nya-x-nyanja_jer_text_reg/19/06.txt

1 line
821 B
Plaintext
Raw Permalink Blame History

This file contains ambiguous Unicode characters

This file contains Unicode characters that might be confused with other characters. If you think that this is intentional, you can safely ignore this warning. Use the Escape button to reveal them.

\v 6 Chifukwa chake taonani, masiku akubwera, watero Yehova, pamene malowo sadzatchedwanso Tofeti, Chigwa cha Beni Hinomu, pakuti adzakhala Chigwa cha Imfa. \v 7 Mmalo muno ndidzasandutsa zolingalira za Yuda ndi Yerusalemu kukhala zopanda pake. Ndidzawagwetsa ndi lupanga pamaso pa adani awo ndi dzanja la anthu amene akufuna moyo wawo. Kenako mitembo yawo ndidzapereka kwa mbalame za mmlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire kuti zikhale chakudya chao. \v 8 Pamenepo ndidzakusandutsa mzinda uno bwinja ndi chinthu chozolitsira mluzu, pakuti aliyense wodutsapo adzanjenjemera ndi kuchita mluzi chifukwa cha miliri yake yonse. \v 9 Ndidzawadyetsa nyama ya ana awo aamuna ndi aakazi; munthu aliyense adzadya mnofu wa mnansi wake mkuwazinga, ndi mkusautsidwa kwa adani ao ndi amene akufuna moyo wao;