1 line
821 B
Plaintext
1 line
821 B
Plaintext
|
\v 6 Chifukwa chake taonani, masiku akubwera, watero Yehova, pamene malowo sadzatchedwanso Tofeti, Chigwa cha Beni Hinomu, pakuti adzakhala Chigwa cha Imfa. \v 7 M’malo muno ndidzasandutsa zolingalira za Yuda ndi Yerusalemu kukhala zopanda pake. Ndidzawagwetsa ndi lupanga pamaso pa adani awo ndi dzanja la anthu amene akufuna moyo wawo. Kenako mitembo yawo ndidzapereka kwa mbalame za m’mlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire kuti zikhale chakudya chao. \v 8 Pamenepo ndidzakusandutsa mzinda uno bwinja ndi chinthu chozolitsira mluzu, pakuti aliyense wodutsapo adzanjenjemera ndi kuchita mluzi chifukwa cha miliri yake yonse. \v 9 Ndidzawadyetsa nyama ya ana awo aamuna ndi aakazi; munthu aliyense adzadya mnofu wa mnansi wake m’kuwazinga, ndi m’kusautsidwa kwa adani ao ndi amene akufuna moyo wao;
|