\v 3 Niziba kuti ndinu banthu olimbikira, elo mwabvutika maningi chifukwa cha zina langa, ndipo simunaleme. \v 4 Koma nili chabe na bvuto imozi pali imwe yakuti mwasiya chikondi chamene munali nacho poyamba. \v 5 Kumbukirani sono kwamene mwagwera. Siyani zoipa na kuchita zamene munali kuchita poyamba. Ngati simuleka zoipa, nizabwera kuchosapo poika nyale kuchoka pa malo pamene ilili.