1 line
409 B
Plaintext
1 line
409 B
Plaintext
\v 4 Ndidzachita zimenezi chifukwa anandisiya ndi kuipitsa malo ano. Pamalo amenewa akupereka nsembe kwa milungu ina imene sankaidziwa. Iwo, makolo awo, ndi mafumu a Yuda adzaza malo ano ndi magazi osalakwa. \v 5 Anamanganso malo okwezeka a Baala kuti atenthe ana awo aamuna pamoto monga nsembe zopsereza za Yehova, chinthu chimene sindinawauze kapena kuwatchula, ndipo sichinalowe m’maganizo mwanga. |