1 line
524 B
Plaintext
1 line
524 B
Plaintext
\v 11 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ndibweretsa tsoka pa iwo, tsoka limene sadzatha kuthawa. Pamenepo adzandiitana, koma sindidzawamvera; \v 12 Mizinda ya Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu adzapita kukafuulira milungu imene anapereka nsembe, koma sadzawapulumutsa pa nthawi ya tsoka lawo. \v 13 Pakuti iwe Yuda, chiwerengero cha milungu yako chachuluka mofanana ndi mizinda yako. Munapanga maguwa ansembe onyansa m’Yerusalemu, maguwa ansembe zofukizira Baala, mofanana ndi kuchuluka kwa misewu yake. |