\v 6 \v 7 Funsani ndikuwona ngati mwamuna abereka mwana. N’chifukwa chiyani ndimaona mnyamata aliyense ali ndi dzanja m’chiuno mwake ngati mkazi wobereka mwana? N’chifukwa chiyani nkhope zawo zonse zatuwa? Tsoka! Pakuti tsikulo lidzakhala lalikulu, lopanda lofanana nalo. Idzakhala nthawi ya nkhawa kwa Yakobo, koma adzapulumutsidwa ku nthawiyo.