\c 3 \v 1 Lomba njoka yenze yocenjera maningi kucila vinyama vonse vamsanga vamene yawe Mulungu anapanga. Anakamba kuli muzimai, " Nanga Mulungu anakamba kuti, ' Musadye kumutengo uliwonse mu munda?" \v 2 Muzimai anauza njoka kuti, " Tingadye cipaso chamu mitenga ya munda, \v 3 koma pali mutengo wamene uli pakati pa munda, mulungu anakamba kuti, ' simungadye, kapena kucigwira, olo muzamwalira.'"